Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 22:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa uli pa ulendo wothamangira kukachita zotsutsana ndi chifuniro changa.+

  • Deuteronomo 33:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndipo anati:

      “Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+

      Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+

      Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+

      Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+

      Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+

  • Salimo 89:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Mulungu ayenera kuopedwa pakati pa gulu lake la oyera.+

      Iye ndi wamkulu ndi wochititsa mantha kuposa onse omuzungulira.+

  • Danieli 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “‘Nditagona pabedi langa, ndinapitiriza kuona masomphenya ndipo ndinangoona mlonda+ woyera+ akutsika kuchokera kumwamba.

  • Danieli 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndiyeno ndinamva woyera winawake+ akulankhula ndipo woyera wina anafunsa woyera amene anali kulankhulayo kuti: “Kodi masomphenya okhudza nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse,+ tchimo lobweretsa chiwonongeko+ ndiponso kupondedwapondedwa kwa malo opatulika ndi kwa khamulo,+ adzakhala a nthawi yaitali bwanji?”

  • Mateyu 18:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo+ kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.+

  • Machitidwe 10:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Tsiku lina cha m’ma 3 koloko masana,*+ anaona mngelo+ wa Mulungu m’masomphenya.+ Mngeloyo anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Koneliyo!”

  • Machitidwe 12:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha,+ chifukwa sanapereke ulemerero kwa Mulungu.+ Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena