21 Mphika uliwonse wakukamwa kwakukulu mu Yerusalemu ndi mu Yuda udzakhala woyera ndipo udzakhala wa Yehova wa makamu. Anthu onse amene azidzapereka nsembe azidzabwera n’kutengako ina mwa miphikayo ndi kuphikiramo.+ Pa tsiku limenelo, m’nyumba ya Yehova wa makamu+ simudzapezeka Mkanani.”+
27 Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa+ ndiponso wabodza,+ sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.+