Mlaliki 12:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakuti Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.+ Yesaya 26:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala kuti adzaimbe mlandu anthu okhala m’dzikoli.+ Magazi amene dzikoli linakhetsa lidzawaonetsa poyera,+ ndipo silidzabisanso anthu amene linapha.”+ Amosi 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+ Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ Chivumbulutso 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+
14 Pakuti Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.+
21 Pakuti taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala kuti adzaimbe mlandu anthu okhala m’dzikoli.+ Magazi amene dzikoli linakhetsa lidzawaonetsa poyera,+ ndipo silidzabisanso anthu amene linapha.”+
2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+