-
Yeremiya 29:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ watero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera m’mitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndakubalalitsirani,’+ watero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani ndi kukupititsani ku ukapolo.’+
-
-
Yeremiya 30:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+
-
-
Amosi 9:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+
-
-
Zefaniya 3:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Pa nthawi imeneyo ndidzakubwezaninso kunyumba anthu inu. Ndithu, pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani pamodzi. Ndidzakuchititsani kukhala otchuka komanso otamandidwa pakati pa mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi. Zimenezi zidzachitika ndikadzabwezeretsa pamaso pako anthu ako amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo,” watero Yehova.+
-