11 M’tsiku limenelo, Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri+ kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,+ ku Hamati ndi m’zilumba za m’nyanja.+
2 Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+