Levitiko 26:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Chotero ndidzakumbukira pangano langa limene ndinachita ndi Yakobo.+ Ndidzakumbukiranso pangano langa ndi Isaki+ komanso ndi Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo. Deuteronomo 4:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuiwala pangano+ la makolo anu limene anawalumbirira. Yesaya 11:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+ monga mmene panalili msewu umodzi umene Aisiraeli anayendamo m’tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo. Yeremiya 23:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+ Ezekieli 11:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera m’mayiko amene ndinakubalalitsirani, ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.”+
42 Chotero ndidzakumbukira pangano langa limene ndinachita ndi Yakobo.+ Ndidzakumbukiranso pangano langa ndi Isaki+ komanso ndi Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo.
31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuiwala pangano+ la makolo anu limene anawalumbirira.
16 Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+ monga mmene panalili msewu umodzi umene Aisiraeli anayendamo m’tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo.
8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+
17 “Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera m’mayiko amene ndinakubalalitsirani, ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.”+