Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 33:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Taonani Ziyoni,+ tauni yathu yochitiramo zikondwerero.+ Maso anu adzaona Yerusalemu, amene ndi malo okhala aphee, opanda chosokoneza chilichonse. Iye ndi hema woti palibe amene adzamuchotse.+ Zikhomo zake sizidzazulidwa ndipo zingwe zake sizidzaduka.+

  • Yesaya 44:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndine amene ndimachititsa mawu a mtumiki wanga kukwaniritsidwa ndiponso amene ndimakwaniritsa mawu onse amene atumiki anga analengeza.+ Ndine amene ndikunena za Yerusalemu kuti, ‘Muzidzakhala anthu.’+ Ndikunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti, ‘Idzamangidwanso,+ ndipo malo ake osakazidwa ndidzawamanganso.’+

  • Yeremiya 31:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhala pamodzi m’dzikolo. Mudzakhalanso alimi ndi anthu oweta ziweto.+

  • Yeremiya 33:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Yehova wanena kuti, ‘Anthu inu mudzanena za dziko lino kuti ndi lopanda pake chifukwa mulibe anthu ndi ziweto. Mudzanena zimenezi za mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu imene yawonongeka,+ moti mulibe anthu ndipo simukukhala munthu aliyense ngakhale ziweto.+

  • Zekariya 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’bwalo la mzinda wa Yerusalemu mudzakhala amuna ndi akazi achikulire.+ Aliyense adzatenga ndodo+ m’dzanja lake pakuti masiku ake adzakhala atachuluka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena