Luka 6:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 “Komanso, lekani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+ Aroma 2:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Choncho munthu iwe,+ kaya ukhale ndani, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira ngati umaweruza ena.+ Pakuti pa nkhani imene ukuweruza nayo wina, ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso woweruzawe+ umachita zomwezo.+ Aroma 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pa chifukwa chimenechi, tisamaweruzane,+ koma m’malomwake tsimikizani mtima+ kuti simuikira m’bale wanu+ chokhumudwitsa+ kapena chopunthwitsa. 1 Akorinto 4:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Chotero musaweruze+ kalikonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike.+ Akadzafika adzaunika zinsinsi za mu mdima+ ndi kuonetsa poyera+ zolingalira za m’mitima, ndipo aliyense adzatamandidwa yekha ndi Mulungu.+
37 “Komanso, lekani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+
2 Choncho munthu iwe,+ kaya ukhale ndani, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira ngati umaweruza ena.+ Pakuti pa nkhani imene ukuweruza nayo wina, ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso woweruzawe+ umachita zomwezo.+
13 Pa chifukwa chimenechi, tisamaweruzane,+ koma m’malomwake tsimikizani mtima+ kuti simuikira m’bale wanu+ chokhumudwitsa+ kapena chopunthwitsa.
5 Chotero musaweruze+ kalikonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike.+ Akadzafika adzaunika zinsinsi za mu mdima+ ndi kuonetsa poyera+ zolingalira za m’mitima, ndipo aliyense adzatamandidwa yekha ndi Mulungu.+