2 Samueli 24:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Davide atawerengadi anthuwo anavutika mumtima mwake.+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano Yehova, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu+ chonde, pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+ Mateyu 26:75 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 75 Tsopano Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+ Luka 18:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+
10 Davide atawerengadi anthuwo anavutika mumtima mwake.+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano Yehova, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu+ chonde, pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+
75 Tsopano Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+
13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+