-
Danieli 4:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
-
-
Danieli 12:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Pamenepo ndinamva mwamuna wovala nsalu uja, amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinje akuyankha. Poyankhapo, anakweza m’mwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere ndi kulumbira+ pa Iye amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzapita nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu, ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.+ Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya+ mphamvu za anthu oyera, zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”
-