Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Fuulani, anthu inu,+ chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.+ Lidzabwera ngati kuti Wamphamvuyonse akulanda zinthu.+

  • Yeremiya 25:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.+ Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda.+ Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’+

  • Ezekieli 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Tsikulo lili pafupi. Inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Limeneli lidzakhala tsiku la mitambo,+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+

  • Yoweli 1:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Kalanga ine! Tsiku lija likufika.+ Tsiku la Yehova lili pafupi.+ Tsikulo lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

  • Yoweli 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova adzalankhula+ pamaso pa asilikali ake ankhondo+ pakuti anthu a mumsasa wake ndi ambiri.+ Amene akukwaniritsa mawu ake ali ndi mphamvu. Tsiku la Yehova ndi lalikulu+ ndi lochititsa mantha. Ndani angaime pa tsiku limeneli?”+

  • Zefaniya 1:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Tsiku limenelo ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lansautso ndi zowawa,+ tsiku la mphepo yamkuntho ndi losakaza, tsiku lamdima wochititsa mantha,+ tsiku lamitambo yakuda ndi lamdima wandiweyani.

  • 2 Petulo 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Muzichita zimenezi poyembekezera+ ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova,+ pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka,+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena