-
Ekisodo 27:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 “Upange guwa lansembe lamatabwa a mthethe,+ mulitali likhale mamita awiri,* ndipo mulifupi likhalenso mamita awiri. Guwalo likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba likhale masentimita 134.+ 2 Upange nyanga mʼmakona ake+ 4. Nyangazo zituluke mʼmakonawo ndipo ulikute ndi kopa.*+
-
-
Ekisodo 30:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 “Upange guwa lansembe zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa amthethe.+ 2 Mbali zake zonse 4 zikhale zofanana, mulitali mwake likhale masentimita 45,* mulifupi mwake masentimita 45. Ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka pamwamba likhale masentimita 90. Nyanga zake azipangire kumodzi ndi guwalo.*+ 3 Ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.
-