Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 4:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pamene mukusamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azikhala atamaliza kuphimba zinthu za mʼmalo oyera+ ndi ziwiya zonse za mʼmalo oyerawo. Kenako ana a Kohati azibwera nʼkudzazinyamula+ koma iwo asamakhudze zinthu za mʼmalo oyerazo chifukwa akatero adzafa.+ Ana a Kohati ndi amene ali ndi udindo wonyamula zinthu zimenezi pachihema chokumanako.

  • Numeri 4:24-26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Anthu amʼmabanja a Agerisoni anapatsidwa ntchito yosamalira ndi kunyamula zinthu izi:+ 25 Azinyamula nsalu za chihema kapena kuti chihema chokumanako,+ nsalu yophimba chihema, chophimba cha chikopa cha katumbu chomwe chili pamwamba pake+ ndi nsalu yotchinga pakhomo la chihema chokumanako.+ 26 Azinyamulanso nsalu za mpanda wa bwalo,+ nsalu yotchinga khomo la mpanda+ umene wazungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zake zonse ndi zinthu zina zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumikiwu. Ntchito imene azigwira ndi imeneyi.

  • Numeri 4:31-33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Zinthu zimene azinyamula,+ mogwirizana ndi utumiki wawo pachihema chokumanako ndi izi: Mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake ndiponso zitsulo zokhazikapo zipilala ndi mafelemu.+ 32 Azinyamulanso zipilala+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki umenewu. Munthu aliyense muzimupatsa katundu woti azinyamula. 33 Izi ndi zimene mabanja a ana a Merari+ azichita monga mbali ya utumiki wawo pachihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni,+ ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena