Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Amos 1:1-9:15
  • Amosi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amosi
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Amosi

AMOSI

1 Awa ndi mawu a Amosi* amene anali mmodzi wa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa mʼmasomphenya okhudza Isiraeli, mʼmasiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi mʼmasiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, kutatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike.+ 2 Iye anati:

“Yehova adzabangula ku Ziyoni,

Ndipo adzafuula ku Yerusalemu.

Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira,

Ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+

 3 “Yehova wanena kuti,

‘“Popeza Damasiko anandigalukira mobwerezabwereza,* sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa anapuntha Giliyadi ndi zida zopunthira zachitsulo.+

 4 Ndidzatumiza moto panyumba ya Hazaeli,+

Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Beni-hadadi.+

 5 Ndidzathyola mipiringidzo ya mageti a Damasiko.+

Ndidzapha anthu a ku Bikati-aveni,

Komanso wolamulira* ku Beti-edeni.

Ndipo anthu a ku Siriya adzapita ku ukapolo ku Kiri,”+ watero Yehova.’

 6 Yehova wanena kuti,

‘“Chifukwa chakuti Gaza+ wandigalukira mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa anatenga anthu onse ogwidwa ukapolo+ nʼkuwapereka ku Edomu.

 7 Ndidzatumiza moto pampanda wa Gaza,+

Ndipo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.

 8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi,+

Komanso wolamulira* wa ku Asikeloni.+

Ndidzalanga Ekironi,+

Ndipo ndidzafafaniza Afilisiti otsala,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’

 9 Yehova wanena kuti,

‘Popeza Turo anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo,

Ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pachibale.+

10 Choncho ndidzatumiza moto pampanda wa Turo,

Ndipo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.’+

11 Yehova wanena kuti,

‘Chifukwa Edomu wandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,+

Komanso anakana kusonyeza chifundo.

Anapitiriza kuwakhadzulakhadzula,

Ndipo anapitirizabe kuwakwiyira kwambiri.+

12 Choncho ndidzatumiza moto ku Temani,+

Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za ku Bozira.’+

13 Yehova wanena kuti,

‘“Chifukwa chakuti Aamoni andigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzawasinthira chigamulo changa.

Chifukwa anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi kuti akulitse malo awo okhala.+

14 Ndidzayatsa mpanda wa Raba,+

Ndipo motowo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.

Padzakhala mfuu ya nkhondo pa tsiku la nkhondo.

Komanso mphepo yamkuntho pa tsiku la chimvula champhamvu.

15 Ndipo mfumu yawo limodzi ndi akalonga ake adzapita ku ukapolo,”+ watero Yehova.’”

2 “Yehova wanena kuti,

‘“Popeza Mowabu anandigalukira mobwerezabwereza,*+ sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa anatentha mafupa a mfumu ya Edomu kuti apeze laimu.

 2 Choncho ndidzatumiza moto ku Mowabu,

Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Kerioti.+

Mowabu adzafa pakati pa phokoso,

Pakati pa mfuu yankhondo ndiponso kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa.+

 3 Ndidzachotsa wolamulira* pakati pake,

Komanso ndidzapha akalonga ake onse limodzi ndi iyeyo,”+ watero Yehova.’

 4 Yehova wanena kuti,

‘Popeza Yuda anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa chakuti anakana malamulo* a Yehova,

Ndiponso chifukwa sanatsatire malangizo ake.+

Koma anasocheretsedwa ndi mabodza amene makolo awo ankatsatira.+

 5 Choncho ndidzatumiza moto ku Yuda

Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Yerusalemu.’+

 6 Yehova wanena kuti,

‘Popeza Isiraeli anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.

Chifukwa chakuti anagulitsa munthu wolungama kuti apeze siliva,

Komanso munthu wosauka kuti apeze nsapato.+

 7 Amapondaponda mitu ya anthu wamba pafumbi,+

Ndipo amatsekereza njira ya anthu ofatsa.+

Bambo ndi mwana wake wamwamuna akugona ndi mtsikana mmodzi,

Ndipo akuipitsa dzina langa loyera.

 8 Zovala zimene alanda anthu ena monga chikole,+ amaziyala pafupi ndi guwa lililonse lansembe+ nʼkugonapo.

Ndipo vinyo amene amakamwera kunyumba* za milungu yawo, amagula ndi ndalama zimene alipiritsa anthu.’

 9 ‘Koma ine ndi amene ndinapha Aamori iwo akuona.+

Aamoriwo anali aatali ngati mitengo ya mkungudza komanso amphamvu ngati mitengo ikuluikulu.

Ndinawononga zipatso zawo mʼmwamba ndiponso mizu yawo pansi.+

10 Ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+

Ndipo ndinakuyendetsani mʼchipululu zaka 40,+

Kuti mukatenge dziko la Aamori.

11 Ndinachititsa ana anu ena kukhala aneneri.+

Ndipo anyamata anu ena ndinawachititsa kukhala Anaziri.+

Si choncho kodi, inu Aisiraeli?’ watero Yehova.

12 ‘Koma inu munkapatsa Anaziri vinyo kuti amwe,+

Ndipo aneneri munawalamula kuti: “Musamanenere.”+

13 Choncho ine ndidzakupondani pamalo anu,

Ngati mmene ngolo imene yanyamula mitolo ya tirigu imapondera zinthu.

14 Munthu waliwiro adzasowa kothawira,+

Palibe munthu wamphamvu amene adzalimbe,

Komanso palibe msilikali amene adzapulumuke.

15 Munthu wokhala ndi uta sadzaima,

Munthu waliwiro kwambiri sadzatha kuthawa

Ndipo wokwera pahatchi* sadzapulumuka.

16 Ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri

Adzathawa ali maliseche pa tsiku limenelo,’+ watero Yehova.”

3 “Tamverani mawu amene Yehova wanena okhudza inu Aisiraeli, mawu okhudza banja lonse limene ndinalitulutsa mʼdziko la Iguputo:

 2 ‘Pa mabanja onse apadziko lapansi, ine ndimadziwa inu nokha.+

Choncho ndidzakulangani chifukwa cha zolakwa zanu zonse.+

 3 Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane kuti akumane?

 4 Kodi mkango umabangula munkhalango usanagwire nyama?

Kodi mkango wamphamvu umalira mʼmalo amene umakhala usanagwire kalikonse?

 5 Kodi mbalame imakodwa pamsampha, pamene palibe msampha?*

Kodi msampha umafwamphuka usanagwire kalikonse?

 6 Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira mumzinda, kodi anthu sanjenjemera?

Kodi tsoka likagwa mumzinda, si Yehova amene wachititsa?

 7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse

Asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+

 8 Mkango wabangula!+ Ndani sakuchita mantha?

Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa walankhula! Ndani sanenera?’+

 9 ‘Lengezani izi pansanja zolimba za ku Asidodi,

Ndiponso pansanja zolimba zamʼdziko la Iguputo.

Munene kuti: “Sonkhanani kuti muukire mapiri a ku Samariya.+

Onani chisokonezo chimene chikuchitika mumzindawu,

Komanso zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo.+

10 Chifukwa sadziwa kuchita zolungama,” watero Yehova,

“Iwo asonkhanitsa chiwawa ndi chiwonongeko munsanja zawo zolimba.”’

11 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,

‘Mdani adzazungulira dziko lonse,+

Ameneyo adzakufoola,

Ndipo adzatenga zinthu munsanja zako zolimba.’+

12 Yehova wanena kuti,

‘Ngati mmene mʼbusa amapulumutsira miyendo iwiri ya chiweto kapena kachidutswa ka khutu mʼkamwa mwa mkango,

Ndi mmenenso adzapulumukire Aisiraeli,

Amene akukhala pamipando yapamwamba* ndiponso kugona pamabedi okongola ku Samariya.’+

13 ‘Tamverani ndipo muchenjeze* nyumba ya Yakobo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Mulungu wa magulu a nkhondo akumwamba.

14 ‘Pa tsiku limene ndidzalanga Aisiraeli chifukwa chondigalukira,+

Ndidzalanganso maguwa ansembe a ku Beteli.+

Nyanga za guwa lansembe zidzadulidwa nʼkugwa pansi.+

15 Ndidzagwetsa nyumba yokhalamo nthawi yozizira ndiponso nyumba yokhalamo nthawi yotentha.’

‘Nyumba zaminyanga ya njovu zidzagwa.+

Ndipo nyumba zikuluzikulu* zidzawonongedwa,’+ watero Yehova.”

4 “Tamverani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basana,

Amene mumakhala mʼphiri la Samariya,+

Inu akazi amene mukuchitira zachinyengo anthu ovutika+ komanso kuphwanya anthu osauka.

Ndipo mumauza amuna* anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’

 2 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mogwirizana ndi kuyera kwake kuti,

‘“Taonani! Masiku adzafika pamene iye adzakukolani ndi ngowe zokolera nyama nʼkukunyamulani.

Ndipo otsala adzawakola ndi mbedza.

 3 Mudzatulukira pamabowo a mpanda amene muli nawo pafupi.

Ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’

 4 ‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa,*+

Bwerani ku Giligala kuti mudzawonjezere machimo.+

Bweretsani nsembe zanu+ mʼmawa.

Ndipo pa tsiku lachitatu, mubweretse chakhumi* chanu.+

 5 Perekani nsembe zoyamikira za mkate wokhala ndi zofufumitsa.+

Ndipo lengezani mokweza za nsembe zanu zaufulu!

Chifukwa nʼzimene mumakonda kuchita, inu Aisiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

 6 ‘Mʼmizinda yanu yonse, ine sindinakupatseni chakudya.

Ndipo ndinachititsa kuti mʼnyumba zanu zonse musakhale chakudya.+

Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

 7 ‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+

Ndinagwetsa mvula mumzinda wina koma mumzinda wina sindinagwetse.

Mvula inagwa mʼmunda umodzi

Koma mʼmunda wina, mmene simunagwe mvula, munauma.

 8 Anthu amʼmizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita mumzinda wina kuti akamwe madzi,+

Ndipo ludzu lawo silinathe,

Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

 9 ‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso matenda a chuku.+

Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina.

Koma dzombe linawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+

Ndipo inu simunabwererebe kwa ine,’+ watero Yehova.

10 ‘Ndinakutumizirani mliri ngati wa ku Iguputo.+

Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+

Ndinachititsa kuti fungo lonunkha lamʼmisasa yanu lifike mʼmphuno mwanu,+

Koma inu simunabwerere kwa ine,’ watero Yehova.

11 ‘Ndinakubweretserani chiwonongeko

Ngati chimene Mulungu anabweretsa ku Sodomu ndi Gomora.+

Ndipo inu munali ngati chikuni cholanditsidwa pamoto.

Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

12 Ndidzakuchitiranso zimenezo, iwe Isiraeli.

Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi,

Konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Isiraeli.

13 Taona! Iye ndi amene anapanga mapiri+ ndipo analenganso mphepo,+

Amafotokozera munthu zimene akuganiza,

Amachititsa kuwala kwa mʼbandakucha kukhala mdima,+

Ndiponso amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+

Dzina lake ndi Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba.

5 “Tamverani mawu awa amene ndikukuuzani monga nyimbo ya pamaliro, inu amʼnyumba ya Isiraeli:

 2 ‘Namwali, Isiraeli, wagwa.

Iye sangathenso kuimirira.

Aliyense wamuthawa nʼkumusiya mʼdziko lake.

Ndipo palibe womudzutsa.’

3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti,

‘Mzinda umene unkapita kunkhondo ndi anthu 1,000, udzatsala ndi anthu 100.

Ndipo mzinda umene unkapita kunkhondo ndi anthu 100, udzatsala ndi anthu 10. Zimenezi ndi zimene zidzachitikire nyumba ya Isiraeli.’+

4 Yehova wauza anthu a mʼnyumba ya Isiraeli kuti:

‘Ndifufuzeni kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+

 5 Musakhale ndi mtima wofuna kupita ku Beteli.+

Ndipo musapite ku Giligala+ kapena ku Beere-seba.+

Chifukwa ndithu Giligala adzapita ku ukapolo.+

Ndipo Beteli adzawonongedwa.*

 6 Funafunani Yehova kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+

Kuti asakuyakireni ngati moto panyumba ya Yosefe.

Nʼkuwotcheratu Beteli popanda wozimitsa motowo.

 7 Mumasandutsa chilungamo kukhala chitsamba chowawa.

Ndipo mumataya pansi chilungamocho.+

 8 Amene anapanga gulu la nyenyezi la Kima ndi gulu la nyenyezi la Kesili,+

Amene amachititsa mdima wandiweyani kukhala kuwala kwa mʼmamawa,

Amene amachititsa masana kukhala ngati mdima wausiku,+

Amenenso amasonkhanitsa madzi amʼnyanja

Nʼkuwakhuthulira pansi,+

Dzina lake ndi Yehova.

 9 Iye adzawononga mwamsanga munthu wamphamvu.

Ndiponso adzawononga malo amene ali ndi mpanda wolimba.

10 Anthuwo amadana ndi munthu wowadzudzula pageti la mzinda,

Komanso amanyansidwa ndi munthu wolankhula chilungamo.+

11 Chifukwa chakuti mumalamula anthu osauka kuti akulipireni akabwereka munda,

Ndipo mumatenga zokolola zawo ngati msonkho,+

Simudzapitiriza kukhala mʼnyumba zamiyala yosema zimene mwamanga.+

Ndiponso simudzamwa vinyo wochokera mʼminda yanu ya mpesa yabwino kwambiri.+

12 Chifukwa ndikudziwa kuchuluka kwa zochita zanu zondigalukira,

Ndiponso kukula kwa machimo anu.

Mumachitira nkhanza munthu wolungama,

Mumalandira ziphuphu,

Komanso mumaphwanya ufulu wa anthu osauka pageti la mzinda.+

13 Choncho anthu ozindikira adzakhala chete pa nthawi imeneyo,

Chifukwa idzakhala nthawi yoopsa.+

14 Yesetsani kuchita zabwino osati zoipa,+

Kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+

Mukatero Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala nanu.

Ngati mmene mwanenera kuti ali nanu.+

15 Muzidana ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.+

Pageti la mzinda pazichitika chilungamo.+

Mwina Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba

Adzakomera mtima mbadwa za Yosefe zotsala.’+

16 Choncho Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Yehova wanena kuti:

‘Padzamveka kulira mʼmabwalo onse a mizinda yanu,

Ndipo mʼmisewu yanu yonse anthu azidzati: “Mayo ine! Mayo ine!”

Adzaitana alimi kuti alire,

Ndiponso akatswiri odziwa kulira maliro kuti alire mokweza.’

17 ‘Padzakhala kulira mokweza mʼminda yonse ya mpesa,+

Chifukwa ine ndidzadutsa pakati panu,’ watero Yehova.

18 ‘Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova!+

Kodi chidzakuchitikireni nʼchiyani pa tsiku la Yehova?+

Limeneli lidzakhala tsiku lamdima, osati kuwala.+

19 Zidzakhala ngati munthu amene akuthawa mkango wakumana ndi chimbalangondo,

Ndipo pamene akulowa mʼnyumba nʼkugwira khoma, njoka ikumuluma.

20 Tsiku la Yehova lidzakhala lakuda, osati lowala,

Lidzakhala lamdima, osati kuwala.

21 Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo sindigwirizana nazo,+

Komanso sindisangalala ndi fungo la nsembe zanu zoperekedwa pamisonkhano yanu yapadera.

22 Ngakhale mutapereka nsembe zathunthu zopsereza ndiponso nsembe zoperekedwa ngati mphatso,

Ine sindidzasangalala ndi nsembe zanuzo.+

Ndipo sindidzakondwera ndi nsembe zanu zamgwirizano zanyama zonenepa.+

23 Siyani kuimba nyimbo zaphokoso,

Ndipo sindikufuna kumva nyimbo zanu zoimbidwa ndi zoimbira za zingwe.+

24 Chilungamo chiyende ngati madzi.+

Ndiponso ngati mtsinje wosaphwa nthawi zonse.

25 Inu amʼnyumba ya Isiraeli,

Kodi pamene munali mʼchipululu muja kwa zaka 40, munandipatsa nsembe zanyama ndi zopereka zina?+

26 Koma inu mudzanyamula Sakuti mfumu yanu ndi Kaiwani,*

Mafano amene munapanga a mulungu wanu wa nyenyezi.

27 Ndipo ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, amene dzina lake ndi Yehova.”+

6 “Tsoka kwa anthu amene akukhala mosatekeseka ku Ziyoni,

Ndiponso anthu amene akuona kuti ndi otetezeka mʼphiri la Samariya.+

Anthu olemekezeka a mtundu wotchuka kuposa mitundu ina,

Amene nyumba yonse ya Isiraeli imapita kwa iwowo.

 2 Pitani mukaone ku Kaline.

Mukakachoka kumeneko mukapite ku Hamati Wamkulu,+

Kenako mukapite ku Gati wa Afilisiti.

Kodi mizinda imeneyi imaposa maufumu anu awiriwa?*

Kapena kodi malo awo ndi aakulu kuposa malo anu?

 3 Kodi inu simukufuna kuganizira za tsiku latsoka?+

Kodi mukufuna kuti chiwawa chikhale paliponse?+

 4 Mumagona pamabedi aminyanga ya njovu+ ndi kudziwongola pamipando yokhala ngati bedi,+

Ndiponso mukudya nkhosa zamphongo komanso ana a ngʼombe* onenepa.+

 5 Mumapeka nyimbo zoti muziimba ndi zeze,*+

Ndipo mofanana ndi Davide, mumapanga zipangizo zoimbira.+

 6 Mumamwera vinyo mʼmakapu akuluakulu,+

Ndipo mumadzola mafuta apamwamba kwambiri.

Komanso simukukhudzidwa* ndi tsoka lomwe linagwera Yosefe.+

 7 Anthu amenewa adzakhala oyambirira kupita ku ukapolo,+

Ndipo phwando laphokoso la anthu ogona modziwongola pamipando yokhala ngati bedi lidzatha.

 8 Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, wanena kuti: ‘Ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndalumbira pa dzina langaʼ+ kuti,

‘Ndimanyasidwa ndi kunyada kwa Yakobo,+

Ndimadana ndi nsanja zake zolimba,+

Ndipo ndidzapereka mzindawu ndi zinthu zake zonse kwa adani ake.+

9 Ngati anthu 10 angatsale mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa. 10 Wachibale* adzabwera kudzawatulutsa nʼkuyamba kuwawotcha mmodzimmodzi. Adzatulutsa mafupa awo mʼnyumbamo, ndiyeno adzafunsa aliyense amene ali mʼzipinda zamkati kuti, “Kodi muli anthu enanso mmenemo?” Ndipo adzayankha kuti, “Mulibe!” Kenako adzamuuza kuti, “Khala chete! Chifukwa ino si nthawi yotchula dzina la Yehova.”’

11 Chifukwa Yehova ndi amene walamula,+

Iye adzagwetsa nyumba zikuluzikulu moti zidzasanduka mulu wadothi.

Ndipo nyumba zingʼonozingʼono zidzasanduka zibuma.+

12 Kodi mahatchi angathamange pathanthwe?

Kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ngʼombe?

Chifukwa mwasintha chilungamo kukhala chomera chapoizoni,

Ndipo mwasandutsa chipatso cha chilungamo kukhala chinthu chowawa.+

13 Mumasangalala ndi zinthu zopanda pake.

Ndipo mukunena kuti: ‘Tapeza mphamvu patokha.’*+

14 Tsopano Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti ‘Inu amʼnyumba ya Isiraeli, ine ndikubweretserani mtundu wa anthu.+

Ndipo udzakuponderezani kuyambira ku Lebo-hamati*+ mpaka kuchigwa* cha Araba.’”

7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, mbewu zomaliza zitayamba kumera.* Zimenezi zinali mbewu zimene ankadzala, akamaliza kumweta udzu wopita kwa mfumu. 2 Dzombelo litamaliza kudya zomera zonse zamʼdziko, ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde khululukani.+ Kodi Yakobo apulumuka bwanji popeza ndi wofooka?”+

3 Choncho Yehova anaiganiziranso nkhaniyi+ ndipo Yehova anati, “Zimenezi sizidzachitika.”

4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsanso masomphenya awa: Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, analamula kuti dziko lilangidwe ndi moto. Motowo unaumitsa madzi akuya ndiponso unawononga kachigawo ka dziko. 5 Ndiyeno ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde musatero.+ Kodi Yakobo apulumuka bwanji popeza ndi wofooka?”+

6 Choncho Yehova anaiganiziranso nkhaniyi+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anati, “Zimenezinso sizidzachitika.”

7 Iye anandionetsanso masomphenya awa: Yehova anaima pamwamba pa khoma limene linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera, ndipo anali ndi chingwe chowongolera mʼmanja mwake. 8 Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Amosi?” Ndinamuyankha kuti: “Ndikuona chingwe chowongolera.” Ndiyeno Yehova anati: “Ndikuika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli, ndipo sindidzawakhululukiranso.+ 9 Malo okwezeka a Isaki+ adzawonongedwa, ndipo malo opatulika a Isiraeli adzasakazidwa.+ Ine ndidzabwera kudzawononga nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.”+

10 Ndiyeno Amaziya wansembe wa ku Beteli,+ anatumiza uthenga kwa Yerobowamu+ mfumu ya Isiraeli wakuti: “Amosi akukukonzerani chiwembu mkati mwenimweni mwa Isiraeli,+ ndipo anthu atopa nawo mawu ake.+ 11 Amosi akunena kuti, ‘Yerobowamu adzaphedwa ndi lupanga ndipo ndithu Isiraeli adzagwidwa mʼdziko lake nʼkutengedwa kupita ku ukapolo.’”+

12 Ndiyeno Amaziya anauza Amosi kuti: “Iwe wamasomphenya, choka, pita kudziko la Yuda. Uzikapeza chakudya* chako kumeneko ndiponso uzikanenera.+ 13 Koma usapitirize kunenera ku Beteli kuno,+ chifukwa ndi malo opatulika a mfumu+ ndiponso nyumba ya ufumuwu.”

14 Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali mʼbusa+ ndiponso wosamalira* nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga kumene ndinkaweta nkhosa ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+ 16 Tsopano imva zimene Yehova wanena, ‘Ukunena kuti: “Usanenere zinthu zoipa zokhudza Isiraeli,+ ndipo usanene mawu alionse+ oipa okhudza nyumba ya Isaki.” 17 Ndiyetu Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu. Ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera mʼdziko lodetsedwa. Isiraeli adzagwidwa ndithu mʼdziko lake nʼkutengedwa kupita ku ukapolo.”’”+

8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinaona dengu la zipatso zamʼchilimwe.* 2 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani Amosi?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona dengu la zipatso zamʼchilimwe.” Kenako Yehova anandiuza kuti: “Mapeto a anthu anga Aisiraeli afika ndipo sindidzawakhululukiranso.+ 3 ‘Pa tsiku limenelo nyimbo za mʼkachisi zidzasanduka kulira mokweza,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Padzakhala mitembo yambiri yotayidwa paliponse+ moti kudzangoti zii!’

 4 Tamvani izi, inu amene mumapondaponda anthu osauka,

Ndiponso amene mumapha anthu ofatsa mʼdzikoli.+

 5 Inu amene mumanena kuti: ‘Kodi chikondwerero cha nthawi imene mwezi watsopano waoneka chitha liti+ kuti tiyambe kugulitsa mbewu zathu?

Sabata+ litha liti kuti tiyambe kutsatsa mbewu zathu,

Kuti tichepetse muyezo wa efa,*

Tiwonjezere kulemera kwa sekeli,*

Komanso kuti tibere anthu ndi masikelo athu achinyengo?+

 6 Litha liti kuti tigule anthu ovutika ndi ndalama za siliva,

Anthu osauka pa mtengo wa nsapato,+

Ndiponso kuti tigulitse mbewu zachabechabe?’

 7 Yehova, amene ndi ulemerero wa Yakobo,+ walumbira mogwirizana ndi dzina lake kuti:

‘Sindidzaiwala zochita zawo zonse.+

 8 Pa chifukwa chimenechi dziko lidzagwedezeka,

Ndipo aliyense wokhalamo adzalira.+

Dziko lonselo lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo,

Nʼkuwinduka, kenako nʼkuphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+

 9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo,

Ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,

Ndiponso kuti mʼdzikolo mugwe mdima dzuwa lisanalowe.+

10 Ndidzasandutsa zikondwerero zanu kukhala maliro.+

Ndipo nyimbo zanu zonse zidzasanduka nyimbo zapamaliro.

Ndidzachititsa kuti anthu onse avale ziguduli ndipo mitu yonse idzametedwa mpala.

Ndidzachititsa kuti zikhale ngati maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekha.

Moti mapeto ake adzakhala ngati tsiku lowawa.’

11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwera

Pamene ndidzatumiza njala mʼdziko.

Osati njala ya chakudya kapena ludzu lofuna madzi,

Koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.+

12 Anthu adzayenda modzandira kuchokera kunyanja mpaka kukafika kunyanja,

Kuchokera kumpoto mpaka kukafika kumʼmawa.

Iwo adzayenda uku ndi uku pofunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.

13 Pa tsiku limenelo anamwali okongola ndiponso anyamata adzakomoka,

Iwo adzakomoka chifukwa cha ludzu.

14 Anthu amene amalumbira pa milungu yonama ya ku Samariya+ nʼkumati:

“Pali mulungu wako, iwe Dani,”+

Ndiponso “pali njira ya ku Beere-seba.”+

Adzagwa ndipo sadzadzukanso.’”+

9 Ndinaona Yehova+ ataima pamwamba pa guwa lansembe ndipo anati: “Menya mutu wa chipilala ndipo maziko ake adzagwedezeka. Udulenso mitu ya zipilala zonse ndipo anthu otsalawo ndidzawapha ndi lupanga. Aliyense amene adzathawa ndidzamuphabe, aliyense amene adzayese kuthawa sadzapulumuka.+

 2 Akadzakumba Manda* kuti abisalemo,

Ndidzawatulutsa ndi dzanja langa.

Ndipo akadzakwera kumwamba,

Ndidzawatsitsira pansi.

 3 Akadzabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,

Ndidzawafufuza mosamala nʼkuwatenga,+

Ndipo akadzathawa pamaso panga nʼkubisala pansi pa nyanja,

Ndidzalamula njoka kuti iwalume pomwepo.

 4 Akadzatengedwa ndi adani awo kupita ku ukapolo,

Kumeneko ndidzalamula lupanga kuti liwaphe.+

Ndidzakhala tcheru kuti ndiwabweretsere tsoka, osati kuwapatsa madalitso.+

 5 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene amakhudza dziko lapansi,

Moti limasungunuka+ ndipo onse okhala mmenemo adzalira.+

Dziko lonse lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo,

Ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.+

 6 ‘Amene amamanga makwerero ake kumwamba,

Nʼkumanga nyumba yake pamwamba pa dziko lapansi.

Ndiponso amasonkhanitsa madzi amʼnyanja

Nʼkuwakhuthulira pansi,+

Dzina lake ndi Yehova.’+

 7 Yehova akufunsa kuti, ‘Inu Aisiraeli, kodi kwa ine simuli ngati anthu a ku Kusi?

Kodi si ine amene ndinatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo,+

Amenenso ndinatulutsa Afilisiti ku Kerete+ komanso Asiriya ku Kiri?’+

 8 Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyangʼana ufumu wochimwawo,

Ndipo ndidzaufafaniza padziko lapansi.+

Koma nyumba ya Yakobo sindidzaifafaniza yonse.’+

 9 ‘Taonani, ine ndikupereka lamulo

Ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Isiraeli pakati pa mitundu yonse,+

Ngati mmene munthu amachitira posefa,

Ndipo mwala sudzadutsa nʼkugwera pansi.

10 Anthu anga onse ochimwa adzaphedwa ndi lupanga.

Amene akunena kuti: “Tsoka silitiyandikira kapena kutigwera.”’

11 ‘Pa tsiku limenelo, ndidzadzutsa nyumba* ya Davide+ imene inagwa,

Ndi kukonza malo amene khoma lake linawonongeka.

Ndidzaikonza kuti isakhalenso bwinja.

Ndipo ndidzaimanga kuti ikhale ngati mmene inalili kale.+

12 Ndidzachita zimenezi kuti anthu anga atenge zinthu zotsala za Edomu.+

Ndiponso za mitundu yonse ya anthu imene inkaitanira pa dzina langa,’ watero Yehova, amene akuchita zimenezi.

13 Yehova wanena kuti, ‘Masiku adzafika,

Pamene wolima adzapitirira wokolola,

Ndipo woponda mphesa adzapitirira wonyamula mbewu.+

Mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera+

Ndipo mʼmapiri angʼonoangʼono muzidzatuluka vinyo wambiri.+

14 Ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+

Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja nʼkumakhalamo.+

Adzalima minda ya mpesa nʼkumwa vinyo wake.+

Adzalimanso minda nʼkudya zipatso zake.’+

15 ‘Ine ndidzawadzala mʼdziko lawo.

Iwo sadzazulidwanso

Mʼdziko limene ndawapatsa,’+ watero Yehova Mulungu wanu.”

Kutanthauza “Kukhala Katundu” kapena “Kunyamula Katundu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chifukwa chondigalukira katatu ndiponso ka 4.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wogwira ndodo yachifumu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wogwira ndodo yachifumu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chifukwa chondigalukira katatu ndiponso ka 4.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “woweruza.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Kapena kuti, “ku akachisi.”

Ena amati “hosi.”

Mabaibulo ena amati, “nyambo.”

Kapena kuti, “pamipando yokhala ngati bedi ya ku Damasiko.”

Kapena kuti, “muchitire umboni wotsutsa.”

Mabaibulo ena amati, “zambiri.”

Kapena kuti, “ambuye.”

Kapena kuti, “mudzandigalukire.”

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Mabaibulo ena amati, “adzakhala malo ochitikira zinthu zamatsenga.”

Nʼkutheka kuti milungu iwiri yonseyi ikunena za pulaneti yotchedwa Saturn, imene ankailambira ngati mulungu.

Ayenera kuti akutanthauza ufumu wa Yuda ndi wa Isiraeli.

Kapena kuti, “ana a ngʼombe amphongo.”

Kapena kuti, “zipangizo za zingwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “simukudwala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mchimwene wa bambo ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tadzitengera nyanga.”

Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Umenewu unali mwezi wa January ndi February.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Uzikadya mkate.”

Kapena kuti, “woboola.”

Mawu akuti “zipatso za mʼchilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina zipatso za kanjedza.

Onani Zakumapeto B14.

Onani Zakumapeto B14.

Amenewa ndi Manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “tenti.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena