Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi, Mwedomu, anapita kwa Sauli kukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+
52 N’chifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa, wamphamvu iwe?+
Kukoma mtima kosatha kwa Mulungu n’kokhalitsa.+
3 Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,+
Umakonda kwambiri kulankhula chinyengo kuposa kulankhula chilungamo.+ [Seʹlah.]
5 Mulungu adzakupasula kosatha.+
Adzakugwetsa ndi kukukokera kunja kwa hema wako,+
Ndipo adzakuzula ndithu m’dziko la anthu amoyo.+ [Seʹlah.]
7 Munthu wamphamvu wotere sadalira Mulungu monga malo ake achitetezo,+
Koma amadalira kuchuluka kwa chuma chake,+
Ndipo chitetezo chake amachipeza m’mavuto amene iyeyo amawachititsa.+