-
Danieli 12:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,+ kalonga wamkulu+ amene waimirira+ kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimirira.+ Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo.+ Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku+ adzapulumuka.+
-
-
Chivumbulutso 17:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Chilombo chimene waona, chinalipo,+ tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho,+ ndipo chidzapita ku chiwonongeko. Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri pochita nacho chidwi. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo+ kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+
-