Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 20:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Tenga ndodoyo,+ ndipo iwe ndi m’bale wako Aroni, musonkhanitse khamu lonse la anthuwo. Muuze thanthwe pamaso pawo kuti litulutse madzi. Utulutse madzi m’thanthweli kuti upatse khamulo, kuti limwe limodzi ndi ziweto zawo.”+

  • Deuteronomo 8:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mungaiwale amene anakuyendetsani m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni,+ zinkhanira ndiponso dziko louma lopanda madzi. Amenenso anakutulutsirani madzi pamwala wolimba ngati nsangalabwi.+

  • Nehemiya 9:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+

  • Salimo 78:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Iye anang’amba miyala m’chipululu+

      Kuti awapatse madzi akumwa ochuluka ngati a m’nyanja.+

  • Salimo 105:41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+

      Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+

  • Salimo 114:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,+

      Ndiponso amasintha mwala wa nsangalabwi kukhala kasupe.+

  • Yesaya 48:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+

  • 1 Akorinto 10:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 ndipo onse anamwa chakumwa chimodzimodzi chauzimu.+ Pakuti anali kumwa pathanthwe lauzimu+ limene linali kuwatsatira, ndipo thanthwelo+ linatanthauza Khristu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena