-
2 Mbiri 8:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Anapereka nsembezo mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku+ loperekera nsembe, malinga ndi chilamulo cha Mose. Nsembezo zinali za pa masabata,+ za pa masiku okhala mwezi,+ ndi za pa zikondwerero zoikidwiratu+ zochitika katatu pa chaka.+ Zikondwererozo zinali chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata,+ ndi chikondwerero cha misasa.+
-
-
Nehemiya 10:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Akazigwiritsire ntchito pokonza mkate wosanjikiza,+ nsembe yachikhalire yambewu,+ nsembe yachikhalire yopsereza ya pa tsiku la sabata+ ndi tsiku lokhala mwezi.+ Akazigwiritsirenso ntchito pokonza madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika+ ndi nsembe yamachimo+ yophimbira machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse za panyumba ya Mulungu wathu.+
-