30 Ndiyeno uike Urimu+ ndi Tumimu m’chovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamalowa kukaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula ziweruzo+ za ana a Isiraeli pamtima pake poonekera kwa Yehova nthawi zonse.
4 Ine ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo,+ ndipo ndinakuwombolani m’nyumba ya akapolo.+ Ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.+