Numeri 13:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Tinaonakonso Anefili,* mbadwa za Anaki,+ moti eni akefe tinangodziona ngati tiziwala kwa iwo. Iwonso ndi mmene anationera.”+ Numeri 14:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pamenepo khamu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anachezera kulira+ usiku wonse. Numeri 32:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Iwo atafika kuchigwa* cha Esikolo+ n’kuliona dzikolo, anatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asakalowe m’dziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+ Deuteronomo 1:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Tipite kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu+ potiuza kuti: “Kumeneko tinaonako anthu akuluakulu, ndiponso aatali kuposa ifeyo,+ ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ Kumeneko tinaonakonso ana a Anaki.”’+ Machitidwe 21:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma Paulo anayankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira+ ndi kunditayitsa mtima?+ Dziwani kuti ine ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa+ ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”
33 Tinaonakonso Anefili,* mbadwa za Anaki,+ moti eni akefe tinangodziona ngati tiziwala kwa iwo. Iwonso ndi mmene anationera.”+
14 Pamenepo khamu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anachezera kulira+ usiku wonse.
9 Iwo atafika kuchigwa* cha Esikolo+ n’kuliona dzikolo, anatayitsa mtima ana a Isiraeli, kuti asakalowe m’dziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+
28 Tipite kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu+ potiuza kuti: “Kumeneko tinaonako anthu akuluakulu, ndiponso aatali kuposa ifeyo,+ ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+ Kumeneko tinaonakonso ana a Anaki.”’+
13 Koma Paulo anayankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira+ ndi kunditayitsa mtima?+ Dziwani kuti ine ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa+ ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”