Oweruza 2:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+ 1 Mafumu 9:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake, anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira. N’chifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+ 2 Mafumu 17:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ana a Isiraeli anachimwira+ Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa m’dziko la Iguputo+ n’kuwachotsa m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, ndipo anayamba kuopa milungu ina.+ 2 Mbiri 7:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira.+ N’chifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+ Yeremiya 19:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+
12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+
9 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake, anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira. N’chifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ana a Isiraeli anachimwira+ Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa m’dziko la Iguputo+ n’kuwachotsa m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, ndipo anayamba kuopa milungu ina.+
22 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira.+ N’chifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
4 Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+