Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 17:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose kuti:+ “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+

  • Numeri 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Tsopano khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ lomwe linali pakati pawo linasonyeza mtima wadyera,+ ndipo ana a Isiraeli nawonso anayamba kulira n’kumanena kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye?+

  • Numeri 16:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iwo anaukira Mose. Oukirawo anali limodzi ndi amuna achiisiraeli okwanira 250. Iwowa anali atsogoleri a anthuwo, owaimira kumisonkhano, amuna otchuka.

  • Numeri 25:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Akaziwo ankabwera kudzaitana Aisiraeliwo kuti azipita nawo limodzi kokapereka nsembe kwa milungu yawo.+ Kumeneko, Aisiraeliwo ankadya ndi kugwadira milungu ya Amowabuwo.+

  • Deuteronomo 31:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga!

  • Deuteronomo 32:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa,+

      Si ana ake, chilemacho n’chawo.+

      Iwo ndiwo m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota!+

  • Nehemiya 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena