Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 23:40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi zikuluzikulu za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi ya m’chigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

  • Deuteronomo 12:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndipo muzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu, chifukwa iye alibe gawo kapena cholowa monga inu.+

  • Deuteronomo 12:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Koma udzazidyera pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova Mulungu wako adzasankhe.+ Udzazidyera pamalowo iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi ndi Mlevi wokhala mumzinda wanu. Ndipo uzidzasangalala+ pamaso pa Yehova Mulungu wako pa zochita zako zonse.

  • Deuteronomo 14:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndalamazo udzagulire chilichonse chimene mtima wako wakhumba,+ kaya ndi ng’ombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa+ ndi chilichonse chimene mtima wako wafuna. Ndipo uzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kukondwera,+ iweyo ndi banja lako.

  • Salimo 32:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.+

      Fuulani ndi chisangalalo inu nonse owongoka mtima.+

  • Salimo 100:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Tumikirani Yehova mokondwera.+

      Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.+

  • Afilipi 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye.+ Ndibwerezanso, Kondwerani.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena