12Ndiyeno amuna a ku Efuraimu anasonkhana pamodzi n’kuwolokera tsidya lina chakumpoto, ndi kuuza Yefita kuti: “N’chifukwa chiyani unawoloka kukamenya ndi ana a Amoni ife osatiitana kuti tipite nawe?+ Tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba yako.”+
41 Pamenepo anthu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “N’chifukwa chiyani+ abale athu a ku Yuda akubweretsani mozemba inu mfumu Davide, pamodzi ndi banja lanu ndi anthu onse amene anali ndi inu kutsidya la Yorodano?”+