Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kenako nzika zonse za Sekemu ndi anthu onse m’nyumba ya Milo+ anasonkhana pamodzi kumene kunali chipilala pafupi ndi mtengo waukulu+ ku Sekemu.+ Kumeneko analonga Abimeleki ufumu.+

  • 2 Mafumu 14:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Yehoasi mfumu ya Isiraeli itamva inamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza+ wa ku Lebanoni, wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija.+

  • Salimo 58:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,+

      Mulungu adzauluza ndi mphepo yamkuntho mitengo yaiwisi yaminga pamodzi ndi imene ikuyaka.+

  • Miyambo 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+

  • Miyambo 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena