-
Oweruza 5:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Kenako anatambasula dzanja lake ndi kugwira chikhomo cha hema.
Anatambasulanso dzanja lake lamanja ndi kutenga nyundo yamtengo, ya anthu ogwira ntchito mwamphamvu.+
Atatero anakhoma Sisera m’mutu ndipo chikhomocho chinatulukira mbali ina ya mutu wakewo.+
Anaphwanya ndi kudula fupa la pafupi ndi khutu la Sisera.
-
-
2 Samueli 11:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndani uja anapha Abimeleki+ mwana wa Yerubeseti?*+ Kodi si mkazi amene anaponya mwala wokhala pamwamba wa mphero+ ali pamwamba pa mpanda, ndipo Abimeleki anafera ku Tebezi+ komweko? N’chifukwa chiyani amuna inu munauyandikira kwambiri mpandawo?’ Pamenepo ukanene kuti, ‘Nayenso Uriya Mhiti, mtumiki wanu, wafa.’”+
-
-
2 Samueli 20:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Nthawi yomweyo, mkaziyo anapita mwa nzeru+ zake kwa anthu onse, ndipo anthuwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri ndi kuuponya kwa Yowabu. Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ moti anthu onse anabalalika kuchoka kumzindawo ndi kupita kwawo. Yowabu nayenso anabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.
-