Ekisodo 21:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.+ Levitiko 24:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Munthu akapundula mnzake, zimene wachitira mnzakezo iyenso muzim’chitira zomwezo.+ Deuteronomo 19:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Diso lako lisamumvere chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.+ 1 Samueli 15:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Koma Samueli anati: “Monga mmene akazi anaferedwera ana awo chifukwa cha lupanga lako,+ momwemonso mayi ako+ aferedwa ana koposa akazi onse.”+ Pamenepo Samueli anadula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.+ Aroma 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+ Agalatiya 6:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+
21 Diso lako lisamumvere chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.+
33 Koma Samueli anati: “Monga mmene akazi anaferedwera ana awo chifukwa cha lupanga lako,+ momwemonso mayi ako+ aferedwa ana koposa akazi onse.”+ Pamenepo Samueli anadula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.+