Yoswa 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+ Rute 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+ Miyambo 17:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+ Miyambo 19:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Chinthu chosiririka mwa munthu wochokera kufumbi ndicho kukoma mtima kwake kosatha,+ ndipo munthu wosauka ali bwino kuposa munthu wonama.+
14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+
8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+
17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+
22 Chinthu chosiririka mwa munthu wochokera kufumbi ndicho kukoma mtima kwake kosatha,+ ndipo munthu wosauka ali bwino kuposa munthu wonama.+