-
2 Mafumu 11:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala+ malinga ndi mwambo wawo. Anaonanso atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba malipenga. Nthawi yomweyo Ataliya+ anang’amba zovala zake n’kuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+
-
-
1 Mbiri 12:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara,+ Zebuloni,+ ndi Nafitali,+ anali kubweretsa chakudya pa abulu,+ ngamila, nyulu* ndi ng’ombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa.+ Anabweretsanso nkhuyu zouma zoumba pamodzi,+ mphesa zouma zoumba pamodzi,+ vinyo,+ mafuta,+ ng’ombe,+ ndi nkhosa.+ Anabweretsa zimenezi zambirimbiri, popeza mu Isiraeli munali chisangalalo+ chachikulu.
-