3 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi amuna inu mwabweradi kudzafunsira kwa ine?+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti inu mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’