1 Samueli 19:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Koma Yonatani, mwana wa Sauli, anali kukonda kwambiri Davide.+ Choncho Yonatani anauza Davide kuti: “Sauli, bambo anga, akufuna kukupha. Chonde, mawa m’mawa ukhale wosamala. Ukakhale pamalo obisika ndipo ukabisalebe choncho.+ 1 Samueli 20:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Choncho Yonatani analumbiranso kwa Davide chifukwa chakuti anali kum’konda kwambiri. Pakuti Yonatani anali kukonda Davide monga mmene anali kudzikondera iye mwini.+ 1 Samueli 20:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+ 2 Samueli 1:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe m’bale wanga Yonatani,Unali wosangalatsa kwambiri kwa ine.+Chikondi chako chinali chapamwamba kwambiri kuposa chikondi cha akazi.+
2 Koma Yonatani, mwana wa Sauli, anali kukonda kwambiri Davide.+ Choncho Yonatani anauza Davide kuti: “Sauli, bambo anga, akufuna kukupha. Chonde, mawa m’mawa ukhale wosamala. Ukakhale pamalo obisika ndipo ukabisalebe choncho.+
17 Choncho Yonatani analumbiranso kwa Davide chifukwa chakuti anali kum’konda kwambiri. Pakuti Yonatani anali kukonda Davide monga mmene anali kudzikondera iye mwini.+
41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+
26 Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe m’bale wanga Yonatani,Unali wosangalatsa kwambiri kwa ine.+Chikondi chako chinali chapamwamba kwambiri kuposa chikondi cha akazi.+