Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Rute 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko,+ ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri+ ngati chinachake kupatulapo imfa chingandilekanitse ndi inu.”

  • 1 Samueli 18:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yonatani ndi Davide anachita pangano,+ chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.+

  • 1 Samueli 19:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma Yonatani, mwana wa Sauli, anali kukonda kwambiri Davide.+ Choncho Yonatani anauza Davide kuti: “Sauli, bambo anga, akufuna kukupha. Chonde, mawa m’mawa ukhale wosamala. Ukakhale pamalo obisika ndipo ukabisalebe choncho.+

  • 1 Samueli 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho Yonatani analumbiranso kwa Davide chifukwa chakuti anali kum’konda kwambiri. Pakuti Yonatani anali kukonda Davide monga mmene anali kudzikondera iye mwini.+

  • 1 Samueli 20:41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+

  • 1 Samueli 23:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yonatani mwana wa Sauli ananyamuka ndi kupita kwa Davide ku Horesi, kuti akalimbikitse+ Davide kudalira Mulungu.+

  • Miyambo 17:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+

  • Miyambo 18:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana,+ koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena