Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 3:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Uike Yoswa kukhala mtsogoleri+ ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa+ anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.’+

  • Nehemiya 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndinawauzanso mmene dzanja+ la Mulungu wanga lachitira zinthu zabwino kwa ine+ ndiponso mawu amene mfumu inandiuza.+ Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timange mpandawo.” Choncho analimbitsa manja awo kuti agwire ntchito yabwinoyi.+

  • Yobu 16:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Ndikanakulimbikitsani ndi mawu a m’kamwa mwanga,+

      Ndipo chitonthozo cha milomo yanga chikanachepetsa . . .

  • Miyambo 17:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse,+ ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.+

  • Miyambo 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mafuta ndi zofukiza zonunkhira+ n’zimene zimasangalatsa mtima, chimodzimodzinso kukoma kwa mnzako chifukwa cha malangizo ake ochokera pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.+

  • Luka 22:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Koma ine ndakupempherera+ iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse+ abale ako.”

  • Machitidwe 15:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ndiponso popeza kuti Yudasi ndi Sila anali aneneri,+ analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.+

  • Aheberi 10:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Tisaleke kusonkhana pamodzi,+ monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane,+ ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena