Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 10:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamenepo atumiki a Farao anamuuza kuti: “Kodi munthu uyu akhala ngati msampha kwa ife kufikira liti?+ Lolani anthuwa apite kuti akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simukudziwabe kuti Iguputo wawonongeka?”+

  • 1 Samueli 18:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiyeno Sauli anauza Davide kuti: “Mwana wanga wamkazi wamkulu Merabu+ alipo. Ndidzakupatsa ameneyu kuti akhale mkazi wako.+ Koma iwe undisonyeze kulimba mtima kwako ndi kumenya nkhondo za Yehova.”+ Mumtima mwake Sauli anati: “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisiti.”+

  • Salimo 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Taonani! Wina ali ndi pakati pa zinthu zoipa,+

      Watenga pakati pa mavuto ndipo ndithu adzabereka chinyengo.+

  • Salimo 38:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+

      Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+

      Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+

  • Miyambo 26:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Munthu wodana nawe amadzibisa ndi milomo yake, koma mkati mwake mumakhala chinyengo.+

  • Yeremiya 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena