Levitiko 19:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “‘Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumachita miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.+ Ine ndine Yehova. 2 Samueli 16:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Tsopano mfumu inafunsa kuti: “Kodi mwana wa mbuye wako ali kuti?”+ Pamenepo Ziba anauza mfumu kuti: “Watsalira ku Yerusalemu, pakuti wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+ Salimo 101:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+Ndimamukhalitsa chete.+Sindingathe kupirira zochita za+Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+ Miyambo 6:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 mboni yachinyengo yonena mabodza,+ ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.+ Miyambo 21:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira.+ Anthu ochita zinthu mwa njira imeneyi akufunafuna imfa.+
16 “‘Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumachita miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.+ Ine ndine Yehova.
3 Tsopano mfumu inafunsa kuti: “Kodi mwana wa mbuye wako ali kuti?”+ Pamenepo Ziba anauza mfumu kuti: “Watsalira ku Yerusalemu, pakuti wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+
5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+Ndimamukhalitsa chete.+Sindingathe kupirira zochita za+Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+
6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira.+ Anthu ochita zinthu mwa njira imeneyi akufunafuna imfa.+