Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Panopa ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga,+ monga momwe Yehova analonjezera Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu m’malo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+

  • 1 Mafumu 6:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Kunena za nyumba ukumangayi, ukayenda motsatira malamulo+ anga ndi kusunga zigamulo+ zanga zonse ndi kuzitsatira,+ inenso ndidzakwaniritsadi mawu anga okhudza iweyo amene ndinalankhula kwa bambo ako Davide.+

  • 1 Mbiri 17:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iye ndiye adzandimangire nyumba,+ ndipo ndithu ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+

  • 1 Mbiri 22:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Iyeyo ndi amene adzamanga nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana+ wanga, ndipo ine ndidzakhala atate wake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu+ pa Isiraeli ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’

  • Zekariya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+

  • Aheberi 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Koma Khristu monga Mwana+ wa mwiniwake wa nyumbayo, anali kuyang’anira nyumba ya Mulungu mokhulupirika. Ife ndife nyumba ya Mulunguyo,+ ngati tagwira mwamphamvu ufulu wathu wa kulankhula ndi kupitirizabe kunyadira chiyembekezocho mpaka mapeto.+

  • 1 Petulo 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa n’kukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera, n’cholinga chakuti mupereke nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena