Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 17:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisiti uja, anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Kodi ameneyu ndi mwana+ wa ndani,+ Abineri?” Poyankha Abineri anati: “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu, ine sindikudziwa ngakhale pang’ono!”

  • 1 Samueli 20:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma poyankha Davide analumbira+ kuti: “Bambo ako ayenera kuti akudziwa ndithu kuti iweyo umandikonda.+ Pa chifukwa chimenechi iwo adzanena kuti, ‘Musamuuze zimenezi Yonatani kuti zingamupweteketse mtima.’ Moti ndikunenetsa, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wako,+ imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+

  • 1 Samueli 25:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+

  • 2 Samueli 14:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Kodi Yowabu+ ndi amene wakutuma?”+ Pamenepo mkaziyo anayankha kuti: “Pali moyo wanu+ mbuyanga mfumu, palibe munthu angapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa zonse zimene inu mbuyanga mfumu mwanena. Mtumiki wanu Yowabu ndi amene wandituma ndi kundiuza zonse zimene ndalankhula nanu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena