-
Oweruza 4:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndiyeno Yaeli mkazi wa Hiberi anatenga chikhomo cha hema ndi nyundo. Kenako analowa m’hemamo, akuyenda monyang’ama n’kukhoma chikhomocho m’mutu mwa Sisera pafupi ndi khutu,+ mpaka chikhomocho chinalowa pansi. Apa n’kuti Sisera ali m’tulo tofa nato ndiponso ali wotopa kwambiri. Mmenemu ndi mmene Sisera anafera.+
-