-
1 Mafumu 22:42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Yehosafati anali ndi zaka 35 pamene anayamba kulamulira. Iye analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili.
-
-
2 Mbiri 20:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha+ zinthu zimene adaniwo anali nazo. Iwo anapeza zinthu zochuluka pakati pa anthuwo monga katundu wosiyanasiyana, zovala ndi zinthu zina zabwinozabwino. Chotero anayamba kutenga zinthuzo mpaka zinawakanika kunyamula.+ Kwa masiku atatu anakhala akututa zofunkhazo chifukwa zinalipo zambiri.
-