16 “Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzaphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira m’dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ monga mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira m’dzina la Baala,+ anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga.+