Numeri 22:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa,+ koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.”+ Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo. 2 Mbiri 18:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Mulungu wanga anene n’zimene ndikalankhule.”+ Yeremiya 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana.’ Koma upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.+ Yeremiya 23:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, alankhule mawu angawo moona.”+ “Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?”+ watero Yehova. Ezekieli 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ 2 Petulo 1:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu,+ koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu+ motsogoleredwa ndi mzimu woyera.+
35 Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa,+ koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.”+ Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo.
13 Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Mulungu wanga anene n’zimene ndikalankhule.”+
7 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana.’ Koma upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.+
28 Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, alankhule mawu angawo moona.”+ “Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?”+ watero Yehova.
4 Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’
21 Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu,+ koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu+ motsogoleredwa ndi mzimu woyera.+