20 Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake. Bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake.+ Chilungamo cha munthu wolungama chidzakhala pa iye,+ ndipo zoipa za munthu woipa zidzakhala pamutu pa woipayo.+