Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 18:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Pa nthawi+ yopereka nsembe yambewu, Eliya mneneri anayandikira guwa lansembelo n’kunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Isiraeli,+ lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli,+ ndi kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+

  • Yesaya 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+

  • Yeremiya 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+

  • Yona 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Anthu okhulupirira mafano, amaleka kusonyeza kukoma mtima kwawo kosatha.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena