-
2 Mafumu 12:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Tsopano wansembe Yehoyada anatenga bokosi+ n’kuboola kachibowo pachivundikiro chake. Kenako anaika bokosilo pambali pa guwa lansembe kumanja, munthu akamalowa m’nyumba ya Yehova. Ansembe omwe anali alonda a pakhomo+ anaika m’bokosilo ndalama zonse+ zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Yehova.
-
-
2 Mbiri 8:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Kuwonjezera pamenepo, Solomo anaika magulu+ a ansembe pa utumiki wawo mogwirizana ndi lamulo la Davide bambo ake.+ Anaikanso Alevi+ pamalo awo a ntchito kuti azitamanda+ ndi kutumikira+ pamaso pa ansembe mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku.+ Komanso anaika alonda a pazipata m’magulu awo kuti akhale m’zipata zosiyanasiyana+ chifukwa ndilo linali lamulo la Davide munthu wa Mulungu woona.
-