Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 9:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iyeyu anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Sauli,+ mnyamata wokongola, ndipo panalibe munthu wina mwa ana a Isiraeli wokongola ngati iyeyu. Sauli anali wam’tali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene anali kum’pitirira m’mapewa ake.+

  • 1 Samueli 10:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiyeno onse amene anali kumudziwa atamuona, anadabwa kuona kuti ali pakati pa aneneri ndipo akulankhula ngati mneneri. Choncho anthuwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi chachitikira mwana wa Kisi n’chiyani? Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+

  • 1 Samueli 11:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli kukhala mfumu pamaso pa Yehova ku Giligalako. Kenako anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova+ kumeneko, ndipo Sauli pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli anali osangalala kwambiri.+

  • 1 Samueli 14:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Tsopano Sauli analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli+ ndipo anamenya nkhondo ndi adani ake onse om’zungulira. Iye anamenyana ndi Mowabu,+ ana a Amoni,+ Edomu,+ mafumu a Zoba+ ndi Afilisiti.+ Kulikonse kumene anali kutembenukira anali kuwalanga.+

  • 1 Samueli 15:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena