Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 11:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli kukhala mfumu pamaso pa Yehova ku Giligalako. Kenako anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova+ kumeneko, ndipo Sauli pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli anali osangalala kwambiri.+

  • 1 Samueli 13:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: “Wachita chinthu chopusa.+ Sunatsatire lamulo+ limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.+ Ukanatsatira lamulo limeneli, Yehova akanalimbitsa ufumu wako pa Isiraeli mpaka kalekale.

  • 1 Samueli 15:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Samueli anamuyankha kuti: “Sindibwerera nawe chifukwa wakana mawu a Yehova, ndipo Yehova wakukana kuti upitirize kukhala mfumu ya Isiraeli.”+

  • 1 Samueli 16:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndiyeno mzimu woipa wa Mulungu ukafika pa Sauli, Davide anali kutenga zeze ndi kumuimbira. Akatero, Sauli anali kupeza bwino, ndipo mzimu woipawo unali kum’chokera.+

  • 1 Samueli 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamapeto pake, Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mkazi waluso polankhula ndi mizimu,+ ndipo ine ndipita kukalankhula naye.” Pamenepo atumiki ake anamuuza kuti: “Ku Eni-dori alipo mkazi waluso polankhula ndi mizimu.”+

  • 1 Samueli 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+

  • 2 Samueli 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Sauli ndi Yonatani,+ anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo,

      Ngakhale pa imfa yawo sanasiyane.+

      Iwo anali aliwiro kuposa chiwombankhanga,+

      Amphamvu kuposa mikango.+

  • Machitidwe 13:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma kuchokera pamenepo anthuwo ananena kuti akufuna mfumu.+ Chotero Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini,+ ndipo anakhala mfumu yawo kwa zaka 40.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena