Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 7:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Pa mapeto pake, Mfumu Solomo inamaliza+ ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene inayenera kugwira. Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zonse zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Anatenga siliva, golide, ndi ziwiya zina n’kukaziika mosungira chuma cha panyumba ya Yehova.+

  • 1 Mafumu 15:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Asa ataona zimenezi anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi pa chuma cha m’nyumba ya mfumu, n’kumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa inatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi+ mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene anali kukhala ku Damasiko.+ Inawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti:

  • 2 Mafumu 25:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa zomwe zinali zagolide weniweni,+ komanso zomwe zinali zasiliva weniweni.+

  • 2 Mbiri 12:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Chotero Sisaki+ mfumu ya Iguputo anaukira Yerusalemu ndi kutenga chuma cha m’nyumba ya Yehova+ ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomo anapanga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena