-
2 Mbiri 14:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Tsopano Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake,+ kuti: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera m’dzina lanu+ kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+
-
-
2 Mbiri 18:31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Iyi ndiyo mfumu ya Isiraeli.”+ Choncho anatembenuka kuti amenyane naye, koma Yehosafati anayamba kukuwa popempha thandizo,+ ndipo Yehova anamuthandiza.+ Nthawi yomweyo Mulungu anawachititsa kuchoka kwa iye.+
-