Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 M’chaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, m’mwezi wachiwiri,+ Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi, ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchitoyo. Kenako anaika Alevi+ m’malo awo kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo kuti akhale oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova.+

  • Ezara 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza.

  • Hagai 1:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndiyeno Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse anayamba kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wawo+ ndi a mneneri Hagai,+ chifukwa Yehova Mulungu wawo anamutuma. Pamenepo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova.+

  • Hagai 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima+ iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova.

      “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’+ watero Yehova.

      “‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa makamu.

  • Zekariya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Pa nthawiyi Satana+ anali ataimirira kudzanja lamanja la Yoswa kuti azim’tsutsa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena