Yobu 34:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona mayendedwe ake onse. Miyambo 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ Yeremiya 16:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+ Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ 1 Petulo 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+
17 Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+